1. Mulungu AKONDA inu ndipo afuna kukupatsani moyo weni-weni wabwino.

Mau a Mulungu atiuzaza....

Cikondi Ca Mulungu
"Pakuti Mulungu anakonda dziko lapansi kotero kuti anapatsa Mwana wace wobadwa yekha , kuti yense waku-khulupilira iye asatayike, koma akhale nao moyo wosatha" (Yohane 3:16).

Mulungu anapatsa moyo weni-weni wa bwino
[Yesu anati] "Nadza ine kuti akhale ndi moyo, ndi kukhala nao ocuruka"  (Yohane 10:10).

Kodi ndi cifukwa ciani anthu ambiri amasowa moyo, ndi kukhala nao ocuruka?
Cifukwa ndi ici...


2. Anthu ndi ocimwa.  Macimo atilekanitsa ndi Mulungu wathu. Cifukwa ca macimo athu sitingathe kuzdiwa Mulungu, ndi kulandira cikondi ca Mulungu, ndi moyo weni-weni wabwino omwe auna kutipatsa.

Anthu onse anacimwa
"Pakuti onse anacimwa, naperewere pa ulemerero wa Mulungu" (Aroma 3:23).

"Koma zoipa zanu zakulekanitsani inu ndi Mulungu wanu: ndipo macimo anu abisa nkhope yace kwa inu, kuti iye sakumva" (Yesaya 59:2)

Talekana ndi Mulungu
Pa ciyambi Mulungu analenga munthu wabwino.  Munthu anakhala bwenzi la Mulungu.  Koma munthu m'meneyo anakana kunvera Mulungu, nacimwa, ndipo analekana ndi Mulungu.  Conco munthu anasandulika mdani wa Mulungu. Cimo litilekanitsa ndi Mulungu...

 

chewa1

Zathu ziperewera
Mulungu ndiye wolungama.  Munthu ndiye wocimwa.  Macimo athu akhala ngati dzenje loopsa lotilekanitsa ndi mulingu.
    Timayesa kufika kwa Mulungu mwa cipembezo cathu, zopereka, ndi zinchito zina. Koma zonse ziperewera kufikitsa kwa Mulungu.
Coona Ca Citatu Citionetsera Njira....


3. Yesu Kristu ndiye njira.  Mwa iye yehka mungathe kudziwa cikondi ca Mulungu, ndi kulandira moyo weni-weni wabwino, umene Mulungu afuna kukupatsani.

Yesu anatifera, naukanso
"Pakuti Kristunso adamva zowawa kamozdi, cifukwa ca macimo, wolungama m'malo mwa osalingama, kuti akatifikitse kwa Mulungu."

Yesu anaukanso
"Yesu ameneyo, Mulungu anamuukitsa; za ici tiri mboni ife tonse"  (Machititdwe 2:32).

Pali njira imodzi yokha
Yesu anati: "Ine ndine njira, ndi coonadi, ndi moyo.  Palibe munthu adza kwa atate koma mwa ine" (Yohane 14:6).

chewa2

Mulungu anatikonzela ulalo.  Yesu Kristu anafa m'malo mwathu kuti iye atiyanjanitse ndi mulungu.

Mwa yesu yekha tingahate kuoloka dzenje ndi kufika kwa Mulungu wotikonda.

Kudziwa Zoona Zitatu izi Sikukwanira, Pofunika...


4. Munthu aliyense pa yekha alandire Yesu Kristu monga Mfumu ndi Mupulumutsi wace.  Mukatero mungathe kulandira cikondi ca Mulungu, ndi moyo weni-weni wabwino umene Mulungu aupatsani.

Ndi cofunikira kulandira Yesu
"Koma onse anamulamdira iye, kwa iwo anapatsa mphamvu yakukhala ana a Mulungu" (Yohane 1:12).

Tilandira Yesu mwa Cikhulupiriro
"Indetu, indetu, ndinena ndi inu.  Iye wokhulupirira ali nao moyo wosathat" (Yohane 6:47).

Tilandira Yesu Kristu pamene tipempha kuti alowe mu mtima mwathu.
[Yesu akuti] "Taona nadima pa khomo, ndi gogogda; wina akamva mau ang nakatsegula pa khomo, ndidzalowa kwa iye, ndipo ndidzadya naye, ndi iye ndi ine" (Cibvumbulutso 3:20).

Kubvomela mau a Yesu Kristu Sikukwanira, pafunika kuti akhale Mpulumitsi ndi Mfumu wa mumtima wanu.

Onani zithunzi-thunzi ziwiri izi:

chewa3

INE
NDITSOGOLELA MOYO
WANGA

INE ndiri pa mpando

Zamoyo zanga zonse zasokonezeka

Yesu ali pa bwalo

 

chewa4

YESU NDIYE MTSOGOLERI WA MOYO WANGA

YESU ndiye mfumu

INE ndine womvera

Za moyo wanga zonse zalongosoka

Kodi ndi cithunzi-thunzi citi comwe cifanizira mtima wanu?
Mufuna kuti mtima wanu ifanane ndi cithunzi-thunzi citi?

Mukhoza kulandila Yesu Kristu tsopano lino:


Ngati mubvomera ndi mtima woona mafunso awa:
Kodi mubvomera kuti muli ocimwa?
Kodi muzindikira kuti inu nokha simukhoza kukonza moyo wanu?
Kodi mukhulupirira kuti Yesu anakuferani kuti mupulumutsidwe?
Kodi mukhulupirira kuti mukampempha Yesu adzalowa mu mtima mwanu?
Kodi mufuna kupempha Ambuye tsopano kuti alowe mtima mwanu, akhale Mpulumusti wanu ndi Mfumu yanu?
Mukhoza kupemhera motere kuti mulandire Yesu

"Ambuye Yesu, ndibvomera kuti ndine wocimwa.  Ndidzindikira kuti pa ine ndeka sindingathe kukonza moyo wanga.  Ndikhulupirira munandifela kuti mundipulumutse.  Ndipempha inu kuti Mulowe mu mtima mwanga tsopano.  Khalani Mpulumitsi wanga ndi mfumu yanga.  Musandulize mtima ndikhale mwana wanu.  Zikomo Ambuye, ndikhulupirira kuti tsopano mwalowa monga munalonjeza mu mau anu.  Amen ."

Kodi mufuna kupemphera motere?

 Pempherani ndipo khulupirani kuti Yesu alowa monga momwe analonjezera.